Hepataitisi AHepataitisi A (matenda omwe poyamba ankatchedwa matenda opatsirana a hepataitisi) ndi matenda opatsirana omwe amagwira chiwindi ndipo amayambitsidwa ndi vailasi yotchedwa hepataitisi A (HAV).[1] Ambiri mwa anthu amene ali ndi mavailasi amenewa, makamaka ana, amasonyeza zizindikiro zochepa kapena sasonyeza n'komwe zizindikiro za matendawa.[2] Kwa anthu amene akusonyeza zizindikiro za matendawa, pamatenga milungu iwiri mpaka milungu 6 kuchokera pamene tizilomboti tinalowa m'thupi kuti zizindikiro ziyambe kuonekera.[3] Nthawi zambiri zizindikiro za matendawa zimaonekera kwa milungu 8 ndipo zina mwa zizindikirozo ndi: nseru, kusanza, kutsegula m'mimba, khungu kuchita chikasu, fkutentha thupi, komanso kumva kupweteka m'mimba.[2] Pafupifupi anthu 10 mpaka 15 pa 100 aliwonse amene asonyeza zizindikiro za matendawa, zizindikirozo zimayambiranso pakatipa miyezi 6 kuchokera pamene tizilombo ta matendawa tinalowa m'thupi.[2] Matendawa amatha kulepheretsa chiwindi kugwira bwino nthcito yake ndipo izi zimachitika makamaka kwa achikulire.[2] Kawirikawiri matendawa amafalikira ngati munthu wadya chakudya kapena kumwa madzi omwe akhudzidwa ndi nyansi za kuchimbudzi zomwe zili ndi tizilombo toyambitsa matendawa.[2] Nkhanu komanso ndiwo zina za m'gulu la nkhanu zomwe sizinaphikidwe mokwanira zimathanso kufalitsa tizilombo toyambitsa matendawa.[4] Matendawa amatha kufalanso ngati munthu yemwe ali ndi matendawa akukhudzana kwambiri ndi anthu ena.[2] Ngakhale kuti ana omwe ali ndi tizolombo toyambitsa matendawa sasonyeza zizindikiro zake, komabe anawo amatha kupatsira anthu ena matendawa.[2] Matendawa akalowa m'thupi la munthu koyamba munthuyo n'kuchira, munthuwo sangadwalenso matendawa kwa moyo wake wonse ngakhale tizilombo tochuluka titalowa m'thupi mwake.[5] Zizindikiro za hepataitisi A n'zofanana ndi zizindikiro za matenda ena ambiri choncho pamafunika kuyeza magazi kuti madokotala atsimikizire ngati munthu ali ndi matendawa.[2] Matenda a hepataitisi alipo mitundu yosiyanasiyana yokwanira 5 motengera mtundu wa vailasi umene umawayambitsa, monga: A, B, C, D, ndi E. Katemera wa hepataitisi A amathandiza kwambiri kupewa matendawa.[2][6] Mayiko ena amalimbikitsa kuti ana onse azilandira katemera wa matendawa nthawi ndi nthawi makamaka ngati ali m'madera amene matendawa ndi ofala kwambiri.[2][7] Zikuoneka kuti munthu akangolandira katemerayu kamodzi, amagwira ntchito m'thupi mwake kwa moyo wake wonse.[2] Matendawa angapewedwe mosavuta potsatira njira zaukhondo monga kusamba m'manja komanso kuphika zakudya m'njira yabwino.[2] Matendawa alibe mankhwala, koma wodwala amapatsidwa mankhwala oti athane ndi zizindikiro za matendawa monga nseru kapena kutsegula m'mimba.[2] Nthawi zambiri munthu yemwe ali ndi tizolombo toyambitsa matendawa amakhala bwinobwino popanda vuto lililonse la chiwindi.[2] Koma ngati matendawa achititsa kut chiwindi chiwonongeke n'kumalephera kugwira bwino ntchito, pangafunike opaleshoni yochotsa chiwindicho n'kuika china.[2] Padziko lonse, anthu 1.5 miliyoni amasonyeza zizindikiro za matendawa chaka chilichonse[2] ndipo zikuoneka kuti anthu mamiliyoni ambirimbiri amatenga tizilombo toyambitsa matendawa.[8] Matendawa ndi ofala kwambiri m'madera amene ukhondo ndi wovuta komanso madzi aukhondo ndi osowa.[7] M'mayiko amene akukwera kumene, pafupifupi ana 90 pa 100 aliwonse amakhala atatenga tizilombo toyambitsa matendawa akamafika pokwanitsa zaka 10 zakubadwa, choncho sangadwale matendawa akafika pa msinkhu wauchikulire.[7] M'mayiko amene ndi olemera ndithu, nthawi zambiri matendawa amafika pokhala mliri chifukwa ana m'mayiko oterewa salandira katemera wa matendawa komanso matupi awo amakhala asanazolowere tizilombo toyambitsa matendawa.[7] Mu 2010, matenda a hepataitisi A anapha anthu okwana 102,000 padziko lonse.[9] Choncho panakhazikitsidwa Tsiku Lokumbukira Matenda a Hepataitisi Padziko Lonse lomwe ndi pa July 28 chaka chilichonse ndipo cholinga chake ndi kuthandiza anthu kuti adziwe za kuopsa kwa matenda a hepataitisi.[7]
|